Exodus 7

1Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Taona ine ndakuyika kuti ukhale ngati Mulungu kwa Farao, ndipo mʼbale wako Aaroni adzakhala mneneri wako. 2Iwe ukanene zonse zimene ndakulamulirazi, ndipo Aaroni mʼbale wako ndiye akaziyankhule kwa Farao kuti atulutse ana a Israeli mʼdziko la Igupto. 3Koma ndidzawumitsa mtima wa Farao, ndipo ngakhale nditachulukitsa zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa mu Igupto, 4iyeyo sadzakumverani. Choncho ndidzakantha Igupto, ndipo ndi ntchito zachiweruzo ndidzatulutsa magulu anga, anthu anga Aisraeli kuwachotsa mʼdziko la Igupto. 5Ndipo Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzatambasula dzanja langa kukantha Igupto ndi kutulutsa Aisraeli mʼdzikomo.”

6Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova anawalamulira. 7Mose anali ndi zaka 80, ndipo Aaroni anali ndi zaka 83 pamene anakayankhula kwa Farao.

Ndodo ya Aaroni Isanduka Njoka

8Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, 9“Ngati Farao adzati kwa inu, ‘Chitani chozizwitsa,’ iwe Mose udzati kwa Aaroni, ‘Tenga ndodo yako ndipo uyiponye pamaso pa Farao,’ ndipo idzasanduka njoka.”

10Kotero Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kuchita monga momwe Yehova anawalamulira. Aaroni anaponya ndodo yake pansi patsogolo pa Farao ndi nduna zake ndipo inasanduka njoka. 11Naye Farao anayitanitsa anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo nawonso amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. 12Aliyense wa iwo anaponya ndodo yake pansi ndipo inasanduka njoka. Koma ndodo ya Aaroni inameza ndodo zawo. 13Koma mtima wa Farao unawuma ndipo sanawamvere monga momwe Yehova ananenera.

Mliri wa Magazi

14Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Farao ndi wowuma mtima. Akukana kulola anthu anga kuti apite. 15Upite kwa Farao mmawa pamene azidzapita ku madzi. Ukamudikire mʼmbali mwa Nailo kuti ukakumane naye ndipo unyamule ndodo imene inasanduka njoka ija mʼdzanja lako. 16Ndipo ukamuwuze Farao kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri wandituma kuti ndikuwuzeni kuti: Lolani anthu anga apite kuti akandipembedze mʼchipululu. Koma mpaka tsopano inu simunandimvere. 17Izi ndi zimene Yehova akunena: Ndi ndodo imene ili mʼdzanja langa ndidzamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi adzasanduka magazi. Ndikadzachita ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova: 18Nsomba za mu Nailo zidzafa, mtsinje udzanunkha ndipo Aigupto sadzatha kumwa madzi ake.’ ”

19Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Tenga ndodo yako uyilozetse ku madzi a mu Igupto pa mitsinje, pa ngalande, pa zithaphwi ndi pa madambo, ndipo onse adzasanduka magazi.’ Mʼdziko lonse la Igupto mudzakhala magazi, ngakhale mʼzotungira madzi zopangidwa ndi mitengo ndi miyala.”

20Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova analamulira. Anakweza ndodo yake pamaso pa Farao ndi akuluakulu ake ndipo anamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi onse anasanduka magazi. 21Nsomba za mu Nailo zinafa ndipo mtsinje unanunkha kwambiri kotero kuti Aigupto sanathe kumwa madzi ake. Magazi anali ponseponse mu Igupto.

22Koma amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. Choncho Farao anawumabe mtima, ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananeneratu. 23Mʼmalo mwake iye anatembenuka ndi kupita ku nyumba yake yaufumu ndipo zimenezi sanazilabadire. 24Anthu onse a ku Igupto anayamba kukumba mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sanathe kumwa madzi a mu mtsinjemo.

Mliri wa Achule

25Panapita masiku asanu ndi awiri Yehova atamenya madzi a mu mtsinje wa Nailo.

Copyright information for NyaCCL